Salmi 129
Molte volte mi hanno oppresso
Nyimbo yoyimba pokwera ku Yerusalemu. “Andizunza kwambiri kuyambira ubwana wanga,” anene tsono Israeli; 2“Andizunza kwambiri kuyambira ubwana wanga, koma sanandipambane. 3Anthu otipula analima pa msana panga ndipo anapangapo mizere yayitali: 4Koma Yehova ndi wolungama; Iye wandimasula ku zingwe za anthu oyipa.” 5Onse amene amadana ndi Ziyoni abwezedwe pambuyo mwamanyazi.
6Akhale ngati udzu womera pa denga la nyumba, umene umafota usanakule; 7sungadzaze manja a owumweta kapena manja a omanga mitolo. 8Odutsa pafupi asanene kuti, “Dalitso la Yehova lili pa inu; tikukudalitsani mʼdzina la Yehova.”
Copiato!
Aa