Salmi 121
Il mio aiuto viene dal Signore
Nyimbo yoyimba pokwera ku Yerusalemu. Ndikweza maso anga ku mapiri; kodi thandizo langa limachokera kuti? 2Thandizo langa limachokera kwa Yehova, wolenga kumwamba ndi dziko lapansi. 3Sadzalola kuti phazi lako literereke; Iye amene amakusunga sadzawodzera.
4Taonani, Iye amene amasunga Israeli sadzawodzera kapena kugona. 5Yehova ndiye amene amakusunga; Yehova ndiye mthunzi wako ku dzanja lako lamanja. 6Dzuwa silidzakupweteka nthawi ya masana, kapena mwezi nthawi ya usiku.
7Yehova adzakuteteza ku zoyipa zonse; adzasunga moyo wako. 8Yehova adzayangʼanira kutuluka kwako ndi kulowa kwako; kuyambira tsopano mpaka muyaya.
Copiato!
Aa