Salmi 112
Beato l'uomo che teme il Signore
Tamandani Yehova. Wodala munthu amene amaopa Yehova, amene amakondwera kwambiri ndi malamulo ake. 2Ana ake adzakhala amphamvu mʼdziko; mʼbado wa olungama mtima udzadalitsidwa. 3Kulemera ndi chuma zili mʼnyumba yake, ndipo chilungamo chake ndi chosatha.
4Ngakhale mu mdima kuwala kumatulukira olungama mtima; wokoma mtima, wachifundo ndi wowongoka mtima. 5Zinthu zabwino zidzabwera kwa iye amene amapereka mowolowamanja ndi wokongoletsa mwaufulu, amene amachita ntchito yake mwachilungamo. 6Ndithu sadzagwedezeka; munthu wolungama sadzayiwalika mpaka muyaya.
7Saopa akamva zoyipa zimene zachitika; mtima wake ndi wokhazikika ndipo amadalira Yehova. 8Mtima wake ndi wotetezedwa, sadzakhala ndi mantha; potsiriza pake adzayangʼana adani ake mwachipambano. 9Wopereka mphatso zake mowolowamanja kwa osauka, chilungamo chake chimanka mpaka muyaya; nyanga yake idzakwezedwa mwaulemu.
10Munthu woyipa adzaona zimenezi ndipo adzapsa mtima; adzakukuta mano ake ndipo adzasungunuka. Zolakalaka za anthu oyipa sizidzachitika konse.