Salmi 100
Servite il Signore con gioia
Salimo. Nyimbo yothokoza. Fuwulani kwa Yehova mwachimwemwe, inu dziko lonse lapansi. 2Mulambireni Yehova mosangalala; bwerani pamaso pake ndi nyimbo zachikondwerero. 3Dziwani kuti Yehova ndi Mulungu. Iye ndiye amene anatipanga ndipo ife ndife ake; ndife anthu ake, nkhosa za pabusa pake.
4Lowani ku zipata zake ndi chiyamiko ndi ku mabwalo ake ndi matamando; muyamikeni ndi kutamanda dzina lake. 5Pakuti Yehova ndi wabwino ndipo chikondi chake ndi chamuyaya; kukhulupirika kwake nʼkokhazikika pa mibado ndi mibado.
Copiato!
Aa