Psalms 111
The beginning of wisdom
Tamandani Yehova. Ndidzathokoza Yehova ndi mtima wanga wonse mʼbwalo la anthu olungama mtima ndi pa msonkhano. 2Ntchito za Yehova nʼzazikulu; onse amene amakondwera nazo amazilingalira. 3Zochita zake ndi za ulemerero ndi zaufumu, ndipo chilungamo chake ndi chosatha.
4Iye wachititsa kuti zodabwitsa zake zikumbukirike; Yehova ndi wokoma mtima ndi wachifundo. 5Amapereka chakudya kwa amene amamuopa Iye; amakumbukira pangano lake kwamuyaya. 6Waonetsa anthu ake mphamvu ya ntchito zake, kuwapatsa mayiko a anthu a mitundu ina.
7Ntchito za manja ake ndi zokhulupirika ndi zolungama; malangizo ake onse ndi odalirika. 8Malamulo ndi okhazikika ku nthawi za nthawi, ochitidwa mokhulupirika ndi molungama. 9Iyeyo amawombola anthu ake; anakhazikitsa pangano lake kwamuyaya dzina lake ndi loyera ndi loopsa.
10Kuopa Yehova ndicho chiyambi cha nzeru; onse amene amatsatira malangizo ake amamvetsa bwino zinthu. Iye ndi wotamandika mpaka muyaya.