시편 133

형제가 연합하여 동거함이 어찌 그리 선하고 아름다운고

Salimo la Davide. Nyimbo yoyimba pokwera ku Yerusalemu. Onani, nʼkokoma ndi kokondweretsa ndithu pamene abale akhala pamodzi mwachiyanjano! 2Zili ngati mafuta amtengowapatali othiridwa pa mutu, otsikira ku ndevu, ku ndevu za Aaroni, oyenderera mpaka mʼkhosi mwa mkanjo wake. 3Zili ngati mame a ku Heremoni otsikira pa Phiri la Ziyoni. Pakuti pamenepo Yehova amaperekapo dalitso, ndiwo moyo wamuyaya.

복사됨!
Aa