시편 123

내가 눈을 들어 주를 우러러보나이다

Nyimbo yoyimba pokwera ku Yerusalemu. Ndikweza maso anga kwa Inu, kwa Inu amene mumakhala kumwamba. 2Taonani, monga momwe maso a akapolo amayangʼana mʼdzanja la mbuye wawo, monga momwenso maso a mdzakazi amayangʼana mʼdzanja la dona wake, choncho maso athu ali kwa Yehova Mulungu wathu, mpaka atichitire chifundo. 3Mutichitire chifundo, Inu Yehova mutichitire chifundo, pakuti tapirira chitonzo chachikulu.

4Ife tapirira mnyozo wambiri kuchokera kwa anthu odzikuza, chitonzo chachikulu kuchokera kwa anthu onyada.

복사됨!
Aa