Salmos 87
Todas mis fuentes están en ti
Salimo la Ana a Kora. Iye wakhazikitsa maziko ake pa phiri loyera; 2Yehova amakonda zipata za Ziyoni kupambana malo onse okhalamo a Yakobo. 3Za ulemerero wako zimakambidwa, Iwe mzinda wa Mulungu: Sela 4“Ndidzanena za Rahabe ndi Babuloni pakati pa iwo amene amandidziwa. Dzikonso la Filisitiya, Turo pamodzi ndi Kusi, ndipo ndidzati, ‘Uyu anabadwira mʼZiyoni.’ ” 5Ndithudi, za Ziyoni adzanena kuti, “Uyu ndi uyo anabadwira mwa iye, ndipo Wammwambamwamba adzakhazikitsa iyeyo.” 6Yehova adzalemba mʼbuku la kawundula wa anthu a mitundu ina: “Uyu anabadwira mʼZiyoni.” Sela 7Oyimba ndi ovina omwe adzati, “Akasupe anga onse ali mwa iwe.”
¡Copiado!
Aa