Salmos 149
La alabanza en la congregación de los santos
Tamandani Yehova. Imbirani Yehova nyimbo yatsopano, matamando ake mu msonkhano wa oyera mtima. 2Israeli asangalale mwa mlengi wake; anthu a ku Ziyoni akondwere mwa Mfumu yawo. 3Atamande dzina lake povina ndi kuyimbira Iye nyimbo ndi tambolini ndi pangwe.
4Pakuti Yehova amakondwera ndi anthu ake; Iye amaveka chipulumutso odzichepetsa. 5Oyera mtima asangalale mu ulemu wake ndi kuyimba mwachimwemwe pa mabedi awo. 6Matamando a Mulungu akhale pakamwa pawo, ndi lupanga lakuthwa konsekonse mʼmanja mwawo, 7kubwezera chilango anthu a mitundu ina, ndi kulanga anthu a mitundu yonse, 8kumanga mafumu awo ndi zingwe, anthu awo otchuka ndi unyolo wachitsulo, 9kuchita zimene zinalembedwa zotsutsana nawo Uwu ndi ulemerero wa oyera mtima ake onse. Tamandani Yehova.